Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 7:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pakuti iye amene izi zineneka za iye, akhala wa pfuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.

14. Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anaturuka mwa Yuda; za pfuko ili Mose sanalankhula kanthu ka ansembe.

15. Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melikizedeke,

16. amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;

17. pakuti amcitira umboni,Iwe ndiwe wansembe nthawi yosathaMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.

18. Pakutitu kuli kutaya kwace kwa lamulo lidadza kalelo, cifukwa ca kufoka kwace, ndi kusapindulitsa kwace,

19. (pakuti cilamulo sicinacitira kanthu kakhale kopanda cirema), ndipo kulinso kulowa naco ciyembekezo coposa, cimene tiyandikira naco kwa Mulungu.

20. Ndipo monga momwe sikudacitika kopanda lumbiro;

21. (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro; koma iye ndi lumbiro mwa iye emeoe ananena kwa iye,Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa,Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).

22. Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 7