Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 7:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Cilevi (pakuti momwemo anthu analandira cilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melikizedeke, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?

12. Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike.

13. Pakuti iye amene izi zineneka za iye, akhala wa pfuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.

14. Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anaturuka mwa Yuda; za pfuko ili Mose sanalankhula kanthu ka ansembe.

15. Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melikizedeke,

16. amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;

17. pakuti amcitira umboni,Iwe ndiwe wansembe nthawi yosathaMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.

18. Pakutitu kuli kutaya kwace kwa lamulo lidadza kalelo, cifukwa ca kufoka kwace, ndi kusapindulitsa kwace,

Werengani mutu wathunthu Ahebri 7