Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 7:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti Melikizedeke uyu, Mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,

2. amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali Mfumu ya cilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiko, Mfumu ya mtendere;

3. wopanda atate wace, wopanda amace, wopanda mawerengedwe a cibadwidwe cace, alibe ciyambi ca masiku ace kapena citsiriziro ca moyo wace, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.

4. Koma tapenyani ukulu wace wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikuru, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.

5. Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira nchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa cilamulo, ndiko kwa abaleao, angakhale adaturuka m'cuuno ca Abrahamu;

6. koma iye amene mawerengedwe a cibadwidwe cace sacokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.

7. Ndipo popanda citsutsano konse wamng'ono adalitsidwa ndi wamkuru.

8. Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamcitira umboni kuti ali ndi moyo.

9. Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzi limodzi la magawo khumi adapereka limodzi la magawo khumi;

10. pakuti pajapo anali m'cuuno ca atate wace, pamene Melikizedeke anakomana naye.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 7