1. Pakuti mkulu wa ansembe ali yense, wotengedwa mwa anthu, amaikika cifukwa ca anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe, cifukwa ca macimo:
2. akhale wokhoza kumva cifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi cifoko;
3. ndipo cifukwa caceco ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe cifukwa ca macimo.