Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 3:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi. Mkuluwansembe wa cibvomerezo cathu, Yesu;

2. amene anakhala wokhulupirika kwa iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yace yonse.

3. Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi.

4. Pakuti nyumba iri yonse iri naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.

5. Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yace yonse, monga mnyamata, acitire umboni izi zidzalankhulidwazi;

6. koma Kristu monga mwana, wosunga nyumba yace; ndife nyumba yace, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa ciye-I mbekezoeo, kucigwira kufikira citsiriziro.

7. Momwemo, monga anena Mzimu Woyera,Lero ngati mudzamva mau ace,

8. Musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo,Monga muja tsiku la ciyesero m'cipululu,

9. Cimene makolo anu anandiyesa naco,Ndi kundibvomereza,Naona nchito zanga zaka makumi anai.

10. Momwemo ndinakwiya nao mbadwouwu,Ndipo ndinati, Nthawi zonse amasocera mumtima;Koma sanazindikira njira zangaiwowa;

Werengani mutu wathunthu Ahebri 3