Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 13:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Potero mwa iye tipereke ciperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo cipatso ca milomo yobvomereza dzina lace.

16. Koma musaiwale kucitira cokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulunguakondweranazo.

17. Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akacite ndi cimwemwe, osati mwacisoni: pakuti ici sicikupindulitsani inu.

18. Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tiri naco cikumbu mtima cokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.

19. Ndipo ndikudandaulirani koposa kucita ici, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.

20. Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye woturuka mwa akufa 1 Mbusa wamkuru wa nkhosa 2 ndi mwazi wa cipangano cosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,

21. 3 akuyeseni inu opanda cirema m'cinthu ciri conse cabwino, kuti mucite cifuniro cacej ndi kucita mwa ife comkondweretsa pamaso pace, mwa Yesu Kristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.

22. Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau acidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwacidule.

23. Zindikirani kuti mbale wathu 4 Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu.

24. Lankhulani 5 atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akulankhulani iwo a ku Italiya.

25. Cisomo cikhale ndi inu nonse. Amen.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 13