Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 13:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cikondi ca pa abale cikhalebe.

2. Musaiwale kucereza alendo; pakuti mwa ici ena anacereza angelo osacidziwa.

3. Kumbukilani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ocitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.

4. Ukwati ucitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi acigololo adzawaweruza Mulungu.

5. Mtima wanu ukhale wosakonda cuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

6. Kotero kuti tinena molimbika mtima,Mthandizi wanga ndiye Ambuye; smdidzaopa;Adzandicitira ciani munthu?

7. Kumbukilani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira citsiriziro ca mayendedwe ao mutsanze cikhulupiriro cao.

8. Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthawi zonse.

9. Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundu mitundu, ndi acilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi cisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo.

10. Tiri nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira cihema alibe ulamuliro wa kudyako.

11. Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, cifukwa ca zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 13