8. Koma ngati mukhala opanda cilango, cimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai.
9. Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?
10. Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa ciyero cace.
11. Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.
12. Mwa ici limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;