Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 12:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Yesu, ameneyo, cifukwa ca cimwemwe coikidwaco pamaso pace, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu,

3. Pakuti talingirirani iye amene adapirira ndi ocimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.

4. Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo cimo;

5. ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana,Mwana wanga, usayese copepuka kulanga kwa Ambuye,Kapena usakomoke podzudzulidwa ndilye;

6. Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga,Nakwapula mwana ali yense amlandira.

7. Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu acitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wace wosamlanga?

8. Koma ngati mukhala opanda cilango, cimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai.

9. Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

10. Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa ciyero cace.

11. Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.

12. Mwa ici limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;

13. ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti cotsimphinaco cisapatulidwe m'njira, koma ciciritsidwe.

14. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

Werengani mutu wathunthu Ahebri 12