Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 11:37-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. 19 anaponyedwa miyala, anacekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda obvala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ocitidwa zoipa,

38. (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi 20 m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.

39. Ndipo iwo onse 21 adacitidwa umboni mwa cikhulupiriro, sanalandira lonjezanolo,

40. 22 popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu opanda ife.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 11