Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 11:33-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. amene mwa cikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anacita cilungamo, analandira malonjezano, 11 anatseka pakamwa mikango,

34. 12 nazima mphamvu ya moto, 13 napulumuka lupanga lakuthwa, 14 analimbikitsidwa pokhala ofok a, anakula mphamvu kunkhondo, 15 anapitikitsa magulu a nkhondo yacilendo.

35. 16 Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo 17 ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,

36. kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi 18 kuwatsekera m'ndende;

Werengani mutu wathunthu Ahebri 11