Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 11:11-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndi cikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yace, popeza anamwerengera wokhulupirika iye amene adalonjeza;

12. mwa icinso kudacokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m'mwamba, ndi ngati mcenga, uli m'mbali mwa nyanja, osawerengeka.

13. Iwo onse adamwalira m'cikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.

14. Pakuti wo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.

15. Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.

16. Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.

17. Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wace wayekha;

18. amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbeu yako idzaitanidwa:

19. poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kucokera komwe, paciphiphiritso, anamlandiranso.

20. Ndi cikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zirinkudza,

21. Ndi cikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yace.

22. Ndi cikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anachula za maturukidwe a ana a Israyeli; nalamulira za mafupa ace.

23. Ndi cikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akumbala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaopa cilamuliro ca mfumu.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 11