Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 10:33-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. pena pocitidwa 5 cinthu cooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ocitidwa zotere.

34. Pakuti 6 munamva cifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa cuma canu, 7 pozindikira kuti muli naco nokha cuma coposa caeikhalire.

35. Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli naco cobwezera mphotho cacikuru.

36. Pakuti cikusowani cipiriro, kuti 8 pamene mwacita cifuniro ca Mulungu, mukalandire lonjezano.

37. 9 Pakuti katsala kanthawi kakang'onong'ono,Ndipowakudzayoadzafika, wesacedwa.

38. 10 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wocokera m'cikhulupiriro:Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwaiye.

39. Koma ife si ndife 11 a iwo akubwerera kulowa citayiko; koma 12 a iwo a cikhulupiriro ca ku cipulumutso ca moyo.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 10