Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 10:3-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Komatu mu izizo muli cikumbukiro ca macimo caka ndi caka.

4. Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndimbuzi ukacotsera macimo.

5. Mwa ici polowa m'dziko lapansi, anena,Nsembe ndi copereka simunazifuna,Koma thupi munandikonzera Ine.

6. Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa macimo simunakondwera nazo;

7. Pamenepo ndinati, Taonani, ndafika,(Pamutu pace pa buku palembedwa za Ine)Kudzacita cifuniro canu, Mulungu,

8. Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa macimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),

9. pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico.

10. Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.

11. Ndipotu wansembe ali yenseamaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo;

12. koma iye, m'mene adapereka nsembe imodzi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire;

13. kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace.

14. Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa.

15. Koma Mzimu Woyeranso aticitira umboni; pakuti adatha kunena,

16. ici ndi cipangano ndidzapangana nao,Atapira masiku ajawo, anena Ambuye:Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;Ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;

17. Ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso.

18. Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwaucimo.

19. Ndipo pokhala naco, abale, cilimbikitso cakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,

20. pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa cocinga, ndico thupi lace;

21. ndipo popeza tiri naye wansembe wamkuru wosunga nyumba ya Mulungu;

22. tiyandikire ndi mtima woona, m'cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Werengani mutu wathunthu Ahebri 10