Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 10:20-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa cocinga, ndico thupi lace;

21. ndipo popeza tiri naye wansembe wamkuru wosunga nyumba ya Mulungu;

22. tiyandikire ndi mtima woona, m'cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

23. tigwiritse cibvomerezo cosagwedera ca ciyembekezo cathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;

24. ndipo tiganizirane wina ndi mnzace kuti tifulumizane ku cikondano ndi nchito zabwino,

25. osaieka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amacita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lirikuyandika.

26. Pakuti tikacimwa ife eni ace, titatha kulandira cidziwitso ca coonadi, siitsalanso nsembe ya kwa macimo,

27. koma kulindira kwina koopsa kwa ciweruziro, ndi kutentha kwace kwa mota wakuononga otsutsana nao.

28. Munthu wopeputsa cilamulo ca Mose angofa opanda cifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:

29. ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa cipangano umene anayeretsedwa nao cinthu wamba, z nacitira cipongwe Mzimu wa cisomo;

30. pakuti timdziwa iye amene anati, 1 Kubwezera cilango nkwanga, loe ndidzabwezera. Ndiponso; 2 Ambuye adzaweruza anthu ace.

31. 3 Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.

32. Koma tadzikumbursani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa 4 mudapirira citsutsano cacikuru ca zowawa;

Werengani mutu wathunthu Ahebri 10