Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 10:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Koma Mzimu Woyeranso aticitira umboni; pakuti adatha kunena,

16. ici ndi cipangano ndidzapangana nao,Atapira masiku ajawo, anena Ambuye:Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;Ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;

17. Ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso.

18. Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwaucimo.

19. Ndipo pokhala naco, abale, cilimbikitso cakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,

20. pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa cocinga, ndico thupi lace;

21. ndipo popeza tiri naye wansembe wamkuru wosunga nyumba ya Mulungu;

22. tiyandikire ndi mtima woona, m'cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

23. tigwiritse cibvomerezo cosagwedera ca ciyembekezo cathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;

24. ndipo tiganizirane wina ndi mnzace kuti tifulumizane ku cikondano ndi nchito zabwino,

25. osaieka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amacita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lirikuyandika.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 10