11. Ndipotu wansembe ali yenseamaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo;
12. koma iye, m'mene adapereka nsembe imodzi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire;
13. kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace.
14. Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa.
15. Koma Mzimu Woyeranso aticitira umboni; pakuti adatha kunena,
16. ici ndi cipangano ndidzapangana nao,Atapira masiku ajawo, anena Ambuye:Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;Ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;
17. Ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso.
18. Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwaucimo.