Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 5:21-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

22. Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro,

23. cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

24. Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace.

25. 1 N gati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

26. 2 Tisakhale odzikuza, outsana, akucitirana njiru.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 5