Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 5:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; cifukwa cace cirimikani, musakodwenso ndi gori la ukapolo.

2. Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Kristu simudzapindula naye kanthu.

3. Ndicitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kucita cilamulo conse.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 5