Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 4:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Koma, Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.

27. Pakuti kwalembedwa,Kondwera, cumba iwe wosabala;Yimba nthungululu, nupfuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala;Pakuti ana ace a iye ali mbeta acuruka koposa ana a iye ali naye mwamuna.

28. Koma ife, abale, monga Isake, tiri ana a lonjezano.

29. Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano,

30. Koma lembo linena ciani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wace, pakuti sadzalowa nyumba mwanawa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.

31. Cifukwa cace, abale, z sitiri ana a mdzakazi, komatu a mfulu.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 4