1. Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse;
2. komatu ali wakumvera omsungira ndi adindo, kufikira nthawi yoikika kale ndi atate wace.
3. Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi;
4. koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wace, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,