Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 3:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwacabe? ngatitu kwacabe.

5. Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nacita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?

6. Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye cilungamo,

7. cotero zindikirani kuti iwo a cikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.

8. Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi cikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.

9. Kotero kuti iwo a cikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo,

10. Pakuti onse amene atama nchito za lamulo Iiwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa,Wotembereredwa ali yense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la cilamulo, kuzicita izi.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 3