23. Koma cisanadze cikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira cikhulupiriro cimene cikabvumbulutsidwa bwino bwino.
24. 1 Momwemo cilamulo cidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, 2 kuti tikayesedwe olungama ndi cikhulupiriro.
25. Koma popeza cadza cikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.
26. 3 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa cikhulupiriro ca mwa Yesu Kristu.
27. 4 Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.
28. 5 Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; 6 pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.
29. Koma ngati muli a Kristu, muli mbeu ya Abrahamu, 7 nyumba monga mwa Lonjezano.