Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 3:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Kristu anaonetsedwa pa maso panu, wopacikidwa?

2. ici cokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?

3. Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?

4. Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwacabe? ngatitu kwacabe.

5. Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nacita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?

6. Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye cilungamo,

7. cotero zindikirani kuti iwo a cikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.

8. Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi cikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.

9. Kotero kuti iwo a cikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo,

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 3