Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 1:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

20. Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.

21. Pamenepo ndinadza ku mbali za Suriya ndi Kilikiya.

22. Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Kristu;

23. koma analinkumva kokha, kuti, iye wakutilondalonda ife kale, tsopane alalikira cikhulupiriroco ada cipasula kale;

24. ndipo analemekeza Mulungu mwaine.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 1