Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 1:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.

12. Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa bvumbulutso la Yesu Kristu.

13. Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Ciyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,

14. ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Ciyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wacangu koposa pa miyambo ya makolo anga.

15. Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa cisomo cace,

16. kuti abvumbulutse Mwana wace mwa ine, kuti ndimlalikire iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsana ndi thupi ndi mwazi:

17. kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.

18. Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.

19. Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

20. Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.

21. Pamenepo ndinadza ku mbali za Suriya ndi Kilikiya.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 1