Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, mtumwi (wosacokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa iye kwa akufa),

2. ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya:

3. Cisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu,

4. amene anadzipereka yekha cifukwa ca macimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano yino yoipa, monga mwa cifuniro ca Mulungu ndi Atate wathu;

5. yemweyo akhale nao ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.

6. Ndizizwa kuti msanga motere mulikutunsika kwa iye amene anakuitanani m'cisomo ca Kristu, kutsata uthenga wabwino wina;

7. umene suli wina; koma pali ena akubvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Kristu.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 1