Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 4:11-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Si kuti ndinena monga mwa ciperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire ziri zonse ndiri nazo.

12. Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

13. Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.

14. Koma munacita bwino kuti munayanjana nane m'cisautso canga.

15. Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'ciyambi ca Uthenga Wabwino, pamene ndinacoka kuturuka m'Makedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a copereka ndi colandira; koma inu nokha;

16. pakuti m'Tesalonikanso munanditumizira pa cosowa canga kamodzi kapena kawiri.

17. Sikunena kuti nditsata coperekaco, komatu nditsata cipatsocakucurukira ku ciwerengero canu.

18. Koma ndiri nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidacokera kwanu, mnunkho wa pfungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.

19. Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa cosowa canu ciri conse monga mwa cuma cace m'ulemerero mwa Kristu Yesu.

20. Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero ku nthawi za nthawi, Amen.

21. Lankhulani woyera mtima ali yense mwa Kristu Yesu. Abalewo akukhala ndiine alankhula inu.

22. Oyera mtima onse alankhula inu, koma makamaka-fwo a banja la Kaisara.

23. Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu cikhale ndi mzimu wanu.

Werengani mutu wathunthu Afilipi 4