Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 3:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundibvuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.

2. Penyererani agaru, penyererani ocita zoipa, penyererani coduladula;

3. pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m'thupi;

4. ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu;

5. wodulidwa tsiku lacisanu ndi citatu, wa mbadwo wa Israyeli, wa pfuko la Benjamini, Mhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;

6. monga mwa cangu, wolondalonda Eklesia; monga mwa cilungamo ca m'lamulo wokhala wosalakwa ine.

7. Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa citayiko cifukwa ca Kristu.

8. Komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale citayiko cifukwa ca mapambanidwe a cizindikiritso ca Kristu Yesu Ambuye wanga, cifukwa ca Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Kristu,

9. ndi kupezedwa mwa iye, wosati wakukhala naco cilungamo canga ca m'lamulo, koma cimene ca mwa cikhulupiriro ca Kristu, cilungamoco cocokera mwa Mulungu ndi cikhulupiriro;

Werengani mutu wathunthu Afilipi 3