Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 2:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ngati tsono muli citonthozo mwa Kristu, ngati cikhazikitso ca cikondi, ngati ciyanjano ca Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,

2. kwaniritsani cimwemwe canga, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala naco cikondi comwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;

3. musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini;

4. munthu yense asapenyerere zace za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzaceo

5. Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,

6. ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,

Werengani mutu wathunthu Afilipi 2