8. Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Kristu Yesu.
9. Ndipo ici ndipempha, kuti cikondi canu cisefukire cionjezere, m'cidziwitso, ndi kuzindikira konse;
10. kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Kristu;
11. odzala nacocipatso ca cilungamo cimene ciri mwa Yesu Kristu, kucitira Mulungu ulemerero ndi ciyamiko.
12. Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidacita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;
13. kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Kristu m'bwalo lonse da alonda, ndi kwa onse ena;
14. ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.
15. Enatu alalikiranso Kristu cifukwa ca kaduka ndi ndeu; koma enanso cifukwa ca kukoma mtima;
16. ena atero ndi cikondi, podziwa kuti anandiika ndicite eokanira ca Uthenga Wabwino;
17. koma ena alalikira Kristu mocokera m'cotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira cisautso m'zomangira zanga.