2. Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.
3. Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;
4. nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndicita pembedzerolo ndi kukondwera,
5. cifukwa ca ciyanjano canu cakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;
6. pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;