Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 1:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO ndi Timoteo, akapolo a Yesu Kristu, kwa oyera mtima onse mwa Kristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:

2. Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.

3. Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;

4. nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndicita pembedzerolo ndi kukondwera,

5. cifukwa ca ciyanjano canu cakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

6. pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;

7. monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndiri nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'codzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'cisomo.

8. Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Kristu Yesu.

9. Ndipo ici ndipempha, kuti cikondi canu cisefukire cionjezere, m'cidziwitso, ndi kuzindikira konse;

Werengani mutu wathunthu Afilipi 1