Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 5:19-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;

20. ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;

21. ndi kumverana wina ndi mnzace m'kuopa Kristu.

22. Akazi Inu, mverani amuna anu ainu eni, monga kumvera Ambuye.

23. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

24. Komatu monga Eklesia amvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna ao m'zinthu zonse.

25. Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m'malo mwace;

26. kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;

27. kutilye akadziikire yekha Eklesia wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda cirema.

28. Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;

29. pakuti munthu sanadana nalo thupi lace ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia;

Werengani mutu wathunthu Aefeso 5