Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 5:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. kuyesera cokondweretsa Ambuye nciani;

11. ndipo musayanjane nazo nchito za mdima zosabala kanthu, koma maka-makanso muzitsutse;

12. pakuti zocitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kucititsa manyazi.

13. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti conse cakuonetsa ciri kuunika.

14. Mwa ici anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndi, po Kristu adzawala pa iwe.

15. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;

16. akucita macawi, popeza masiku ali oipa,

17. Cifukwa cace musakhale opusa, koma dziwitsani cifuniro ca Ambuye nciani.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 5