Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 5:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa;

2. ndipo yendani m'cikondi monganso Kristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, copereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale pfungo lonunkhira bwino.

3. Koma dama ndi cidetso conse, kapena cisiriro, zisachulidwe ndi kuchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

4. kapena cinyanso, ndi kulankhula zopanda pace, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka ciyamiko.

5. Pakuti ici mucidziwe kuti wadama yense, kapena wacidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe colowa m'ufumu wa Kristu ndi Mulungu.

6. Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pace, pakuti cifukwa ca hi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

7. Cifukwa cace musakhale olandirana nao;

8. pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,

9. pakuti cipatso ca kuunika ticipeza m'ubwino wonse, ndi cilungamo, ndi coonadi,

10. kuyesera cokondweretsa Ambuye nciani;

Werengani mutu wathunthu Aefeso 5