Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 4:29-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. 8 Nkhani yonse yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, 9 kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva.

30. Ndipo 10 musamvetse cisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa cizindikilo mwa iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

31. 11 Ciwawo conse, ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi ciwawa, ndi mwano zicotsedwe kwa inu, ndiponso coipa conse.

32. Koma 12 mukhalirane okoma wina ndi mnzace, a mtima wacifundo, akukhululukirana nokha, 13 monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 4