Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 4:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za cinyengo;

23. koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,

24. 2 nimubvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'cilungamo, ndi m'ciyero ca coonadi.

25. Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace; 4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace.

26. 5 Kwiyani, koma musacimwe; dzuwa lisalowe muli cikwiyire,

27. ndiponso 6 musampatse malo mdierekezi.

28. Wakubayo asabenso; koma 7 makamaka agwiritse nchito, nagwire nchito yokoma ndi manja ace, kuti akhale naco cakucereza wosowa.

29. 8 Nkhani yonse yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, 9 kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva.

30. Ndipo 10 musamvetse cisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa cizindikilo mwa iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

31. 11 Ciwawo conse, ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi ciwawa, ndi mwano zicotsedwe kwa inu, ndiponso coipa conse.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 4