Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 4:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,

2. ndi kuonetsera kudzicepetsa konse, ndi cifatso, ndi kuonetsera cipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzace, mwa cikondi;

3. ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa cimangiriro ca mtendere.

4. Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'ciyembekezo cimodzi ca maitanidwe anu;

5. Ambuye mmodzi, cikhulupiriro cimodzi, ubatizo umodzi,

6. Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.

7. Ndipo kwa yense wa ife capatsika cisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu.

8. Cifukwa cace anena,M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,Naninkha zaufulu kwa anthu.

9. Koma ici, cakuti, Anakwera, nciani nanga komakuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?

Werengani mutu wathunthu Aefeso 4