Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 3:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. umene anandikhalitsa mtumiki wace monga mwa mphatso ya cisomo ca Mulungu, cimene anandipatsa ine, monga mwa, macitidwe a mphamvu yace.

8. Kwa ine wocepa ndi wocepetsa wa onse, oyera mtima anandipatsa cisomo ici, ndilalikire kwa amitundu cuma cosalondoleka ca Kristu;

9. ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a cinsinsico, cimene cinabisika ku yambira kale kale mwa Mulungu wolenga zonse;

10. kuti mu Eklesia azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,

11. monga mwa citsimikizo mtima ca nthawi za nthawi, cimene anacita mwa Kristu Yesu Ambuye wathu:

12. amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa cikhulupiriro ca pa iye.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 3