Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 3:18-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera,

19. ndi kuzama nciani; ndi kuzindikira cikondi ca Kristu, cakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira cidzalo conse ca Mulungu.

20. Ndipo kwa iye amene angathe kucita koposa-posatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kucita mwa ife,

21. kwa iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Kristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 3