Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 3:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Mwa ici ndipempha kuti musade mtima, m'zisautso zanga cifukwa ca inu, ndiwo ulemerero wanu.

14. Cifukwa ca ici ndipinda maondo anga kwa Atate,

15. amene kucokera kwa iye pfuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alicha dzina,

16. kuti monga mwa cuma ca ulemerero wace akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wace, m'kati mwanu,

17. kuti Kristu akhale cikhalire mwa cikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'cikondi,

18. mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera,

19. ndi kuzama nciani; ndi kuzindikira cikondi ca Kristu, cakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira cidzalo conse ca Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 3