Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 3:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa ca ici ine Paulo, ndine wandende wa Kristu Yesu cifukwa ca inu amitundu,

2. ngatitu munamva za udindo wa cisomo ca Mulungucimene anandipatsa ine ca kwa inu;

3. ndi umo anandizindikiritsa cinsinsico mwa bvumbulutso, monga ndinalemba kale mwacidule,

4. cimene mukhoza kuzindikira naco, pakuciwerenga, cidziwitso canga m'cinsinsi ca Kristu,

5. cimene sanacizindikiritsa ana a anthu m'mibadwo yina, monga anacibvumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ace oyera mwa Mzimu,

6. kuti amitundu ali olowanyumbapamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi oland ira nafe pamodzi palonjezano mwa Kristu Yesu, mwa Uthenga Wabino,

7. umene anandikhalitsa mtumiki wace monga mwa mphatso ya cisomo ca Mulungu, cimene anandipatsa ine, monga mwa, macitidwe a mphamvu yace.

8. Kwa ine wocepa ndi wocepetsa wa onse, oyera mtima anandipatsa cisomo ici, ndilalikire kwa amitundu cuma cosalondoleka ca Kristu;

9. ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a cinsinsico, cimene cinabisika ku yambira kale kale mwa Mulungu wolenga zonse;

10. kuti mu Eklesia azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,

Werengani mutu wathunthu Aefeso 3