Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 1:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire iye;

18. ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero wacolowa cace mwa oyera mtima,

19. ndi ciani ukuru woposa wa mphamvu yace ya kwa ife okhulupira, monga mwa macitidwe a mphamvu yace yolimba,

20. imene anacititsa mwa Kristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, 1 namkhazikitsa pa dzanja lace lamanja m'zakumwamba,

21. 2 pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lochedwa, si m'nyengo yinoya pansi pano yokha, komanso mwaiyo ikudza;

22. ndipo 3 anakonza zonse pansi pa mapazi ace, nampatsa iye 4 akhale mutu pamtu pa zonse,

23. 5 kwa Eklesia amene ali thupi lace, 6 mdzazidwe wa iye amene adzazazonse m'zonse.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 1