Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

3 Yohane 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. MKURUYO kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'coonadi.

2. Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera,

3. Pakuti ndinakondwera kwakukuru, pofika abale ndi kucita umboni za coonadi cako, monga umayenda m'coonadi.

4. Ndiribe cimwemwe coposa ici, cakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m'coonadi.

5. Wokondedwa, ucita cokhulupirika naco ciri conse, uwacitira abale ndi alendo omwe;

6. amene anacita umboni za cikondi cako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzacita bwino:

7. pakuti cifukwa ca dzinali anaturuka, osalandira kanthu kwa amitundu.

Werengani mutu wathunthu 3 Yohane 1