11. Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi iye, tidzakhalanso moyo ndi iye:
12. ngati ttpirira, tidzacitanso ufumu ndi iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:
13. ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sakhoza kudzikana yekha.
14. Uwakumbutse izi, ndi kuwacitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asacite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.