Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Petro 1:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo tiri nao mau a cinenero okhazikika koposa; amene mucita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukaca, nikauka nthanda pa mtima yanu;

20. ndi kudziwa ici poyamba, kuti palibe cinenero ca lembo citanthauzidwa pa cokha,

21. pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

Werengani mutu wathunthu 2 Petro 1