Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Atesalonika 3:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Y esu Kristu, kuti agwire nchito pokhala cete, nadye cakudya cadwo okha,

13. Kama inu, abale, musaleme pakucita zabwino.

14. Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata uyu, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti acite manyazi.

15. Koma musamuyese mdani, kama mumuyambirire ngati mbale.

16. Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.

17. Cilankhulo ndi dzanja langa Paulo; ndico cizindikilo m'kalata ali yense; ndiko kulemba kwanga.

18. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.

Werengani mutu wathunthu 2 Atesalonika 3