Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Atesalonika 3:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;

2. ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenerandi oipa; pakuti si onse ali naco cikhulupiriro.

3. Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

4. koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumacita, ndiponso mudzacita zimene tikulamulirani.

5. Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'cikondi ca mulungu ndi m'cipiriro ca Kristu,

6. Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti mubwebvuke kwa mbale yense wakuyenda dwacedwace, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.

7. Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwacedwace mwa inu;

8. kapena sitinadya mkate cabe pa dzanja la munthu ali yense, komatu m'cibvuto ndi cipsinjo, tinagwira nchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu;

9. si cifukwa tiribe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu citsanzo canu, kuti mukatitsanze ife.

10. Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ici, Ngati munthu safuna kugwira nchito, asadyenso.

Werengani mutu wathunthu 2 Atesalonika 3