Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 7:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsirfza ciyero m'kuopa Mulungu.

2. Tipatseni malo; sitinamcitira munthu cosalungama, sitinaipsa munthu, sitinacenjerera munthu.

3. Sindinena ici kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.

4. Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga cifukwa ca inu nkwakukuru; ndidzazidwa naco citonthozo, ndisefukira naco cimwemwe m'cisautso cathu conse.

5. Pakutinso pakudza ife m'Makedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.

6. Koma iye amene atonthoza odzicepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwace kwa Tito;

7. koma si ndi kufika kwace kokha, komanso ndi citonthozo cimene anatonthozedwa naco mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, cangu canu ca kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa,

8. Kuti ngakhale ndakumvetsani cisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani cisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.

9. Tsopano ndikondwera, sikuti mwangomvedwa cisoni, koma kuti mwamvetsedwa cisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kali konse.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 7